Anti Ahmadiyya Movement in Islam BISM ILLAH RAHMAN RAHIM
AlFatwa International No. 8
Chi*****wa nchiyani ndinasiya Ahmadiyyah? Mutendere Ukhare kwa Allah, Umodzi yekha Chikondi ndi wa Allah wotsatha Ukhare pa Mtumiki Muhammad, Banja lake ndi Omutsatira.
By Dr Ismail A.B. Balogun
Amene Anali Mkulu wa Ahmadi
“.... Ine ndinena kuti, pambuyo pa mulungu ndi munthu, ndi taona makambidwe a Ahmadiyyah, ndapeza kuti akusochoneza anthu cabe ndiponso akusewera ndi ku saziwa kwa chisilamu kwao.“Dr Balogun
M’malemba ambiri amene aturusidwa mukati mwa Nigeria mu nthawi ya 1974, Dr Ismail A.B Balogu, anali ndi udindo wa ukulu mimpingo. Iye analemba ku onetsa boza la mpingo umene anabadwiramo ndiponso umene anakuliramo. Iye anali Professor wa Chisilamu ndiponso wa Ibadan mu Nigeria. Dr Balogun anapereka umoyo wace wonse pa Ahmadiyyah ndiponso anakhala kazembe wa mpingo umenewu kwa dzaka zambiri. Mayakhulindwa ace ndi kuchoka kwace m’mpingo kuna lengetsa anthu ambiri ophuzira kuona kusowa kwa chazoona ndi kusiyana kwace ndi Ahmadiyyah.
Allah amamvomera ma pemphero ya anthu ochimwa amene apempha chikhulukiriro pa mbuyo pochita zoipa chi*****wa chosaziwa Allah (SWT) apereka chifundo cace. Allah (SWT) ndiwanzeru ndi wachilamuriro
(Qur’an An-Nisa 4:17)
Dr Balogun anaika muzele wa zi*****wa zimene zinalenga kuti achoke mphingo wa Ahmadiyyah ndiponso analemba bukhu lotsusani pakati pa chisilamu ndi Ahmadiyyah lochedwa ‘Islam versus Ahmadiyya’ mukati kwa Nigeria. Mu bukhu lace, Dr Bulogun iye ndi ena anthu ophunizira anamizididwa ndi maphungu a Ahmadiyyah ndiponso anamvomera mphingo umenewu chi*****wa chomvesera makolo ao. Siapa pokha ai, iwo anamizidwa ndi akulu amphingo umeneu pa nchito zao zambiri ku Pakistani kuja.
Dr Balogun anaika mundandanda pakula kwace ndi munene iye anakhalira ndi chikhulupiriro mu Pakstani Ahmadi monga mmene analembera mu bukhu lace.
“ Pa Umwana wanga, ndinakula ndi ganizo lokhurupirira mu Indo-Pakistani Ahmadiyyah pa usogoleri wace ndi zichitidwe za m’mphingo wonse. Pamene mphingo unapasidwa kwa akulu, anaupatsa kwa ife, kuti tikhulupirire za zaoona.
Tinamvomera zonse zimene anali kutiuza ndi kuti phunitsa kulingana ndi mkangano wao ndi Chisilamu,kuti ife tikhulupirire amene anali kutiuza.
Ganizo lao linari lochotsa ife muchisilamu chimene iyo anapezano zobvuto munene anali ku chiyendetsera.
Iwo anaziitano kuti ndi asilimu achoonadi ndiponso naziitana nati ndi ‘Ahmadiyyah.”
Iyo nthawi zambiri, anatiuza ku mvutika kumene anthu Ahmadiyya anapeza mu lndia ndiponso ku Pakistani. Iwo anati kulibe mtumiki amene anthu anamukonda M’nzinda wace. Ici cinawapangitsa ku manga fundi yao.”
(Islam Versus Ahmadiyyah in Nigeria p.85-86)
Patapita zaka zambiri, Dr Balogun anaotsa ganizo lace lokana kuti akhale munthu wa mkulu mu Pakistani Ahmadi ndiponso kuti azisokoneza anthu. Anthu amene awa ziphunzitsidwe zao sizionetsa chithunzi choera ndiponso maganizo ace; chi*****wa mwa izi nchito yao ndi kusokoneza Asilamu amene saziwa kali konse. Dr Balogun ananena zimenezi mubukhu lace nati:
“Ngakhale Ahmadiyya yakhala mdziko lino kwa dzaka zokwanira 60 years, ndaona kuti anthu ambiri amene ali mu Guluri sakuziwa chimene akuchita,. Kwa chisanzo, ndi kwatsopano pamene Ahmadiyyah amveka kwambiri.
Iwo akulu a Ahmadis anaziwa kuti. Mirza Ahmad anali kunena kuti ndi mkumiki pa chiyambi.”
(Ibid. P.3)
[Zoona ndi zakuti Ahmadis akhara obitsa chisinsi]
zionetsero za guru limeneri ndi zakuti mwana Imodzi anachoka kwao ku Nigeria ku kachika maphunziro apamwamba ku Britani. Pamene anali kumeneku anakumana ndi wina wa chimwenye amene anali Mu Ahmadiyyah. Mwanayu anatsata zikhalidwe za munthuyu ndiponso pamene anabwera ku Nigeria anasiya mpingo umeneu. Iye anali madalitso amalemu Al-Haj L.B Ahusto” (Ibid. P.2)
Kuchokera pa chiyambi anthu a Ahmadiyyah asewenzetsa njira za christu zonyegeramo anthu ku akhalitsa ngati anthu ao. Iwo asokoneza asilamu ambiri-mbiri pambuyo poti awasata. Akuziwa kuti anthu amene anakhara m’mambari ao kale ndi kuwauza kuti ataye mphingo umeneu ngakhala akuona kuti mphingo umenewu siukunena zazoona.
Zoonadi anapeza atate ao ali munjira yokhota, ndiye naiwo atsata mapazi awo. Ndiponso ambiri mwa iwo asochera (Qur’an As-saffat 37:69-71)
Dr balogun ananena nati, Muchaka cha 1974, Boma la Pakistani ndi guru lochedwa Muslim World League ananena kuti guru la anthu a Ahmadiyyah sasilamu ayi . Iye Dr Balogun anayetsa kwa mpamvu zace zonse kuonetsa kuti bungwe limeneri linali la asilamu, koma izi zinakanika. Pamene anayangana kaphunzisidwe ndi malemba ao Ahmadiyya, Iye Dr Balogun anakhara ndi ganizo lotaya mphingo umene anabadwiramo ndi ku kuliramo nakhara musilamu wa choonadi. Ngakhale kuti Dr Balogun anali mkulu-mkulu wa Ahmadiyyah, iye anakhala munthu wao kwa dzaka zokwanira 40 years kopanda ku dziwa chisinsi cace cha Ahmadiyyah.
Kulingana ndi malembedwe ya Ahmadi Mishoni kuchokera mu Qu’ran, Mahaditsi ndiponso malembedwe ya asilamu ena, Dr Balogun ananena nati:
“ Lingo lao (pa kuona zilembedwe zoperekedwa ndi Ahmadi) inali kuti ndi zilimbitse ndiponso ndi menyana ndi adani a Ahmadiyyah; Koma mwa nzeru ndi naona kuti chikhulupiriro changa chiyenera ku khara nsanda yanga. Pa kuti ine ndine mkulu wa mphunziro pa University ndiye kuti kofunika kuti ndi khare ndi choonadi cha Ahmadiyyah.
M’kuona kwanga ndiponso kuyangana m’bukhu amene Ahmadiyya atenga umboni wao ndapedza kuti zambiri zindikhumudwitsa..…
Ndinena pamatso pa Mulungu ndi munthu kuti zimene Ahmadiyyah a kunena ndi zabooza ndiponsa iwo akunamiza anthu ambiri pa dziko Lapasi. Anthu ambiri amene awatsata saziwa chimene akucita.
Pa nthawi zambiri ndi kulemba zimene a kalembera amabukhu ambiri ananena. Iwo akututsa zimene Ahmadiyyah ananena. Anthu a Ahmadiyya a kuonetsa kuti akalembera amabukuwa amvomekeza zimene akunena koma pambuyo pace akunama chabe.... ndi kuona zimene Ahmadis analemba ndiponso amanena ndiye pamene booza yao iwoneka poyera. Izi zionetsa m’mene anthu a Ahmadiyyah a ku Pakistani anamira anthu” (Ibid p.86-87)
Dr Balogun anapeza kuti amene anayamba mphingo wa Ahmadiyyah ndi akulu-akulu m’gulu limeneri akunama anthu ndi mbiri yao imene akufalitsa. M’ bukhu lace akunena kuti:
“ Zioonetsa poyera kuti malembedwe ya anthu a Ahmadiyyah ndiyobooza ndiponso a kusutsa malemba ya anthu amene a kunena kuti athokoza zolemba zao. Pa nkhani ya akalembera amabuku zionetsa kuti a kuchi kaduka kwa anthu olemba mabuku awo. Chintu chomwe sichivomezedwa pa nkhani ya anthu olemba mabuku pa dziko lapasi ndi kunamiza akalembera ena pa nkhani ya malembedwe. Mwa chinsanzo Quran 2:59 (ndiponso 7:162) kuti: “Abooza asitha malembedwe amene analembedwa; mwa izi tathaudwe kuchotsa anthu asochere.” Ichi ndi chakudya cha ganizo la Ahmadis (Ibid p.94-95)
Ndi ao amene sakhulupira muzitsazo za Allah, ndiwo amene a kuchimwa anamizira bukhu Loyera( Quran An-Nahl, 16:105)
Ma Ahmadiyyah ambiri ku Pakistani Sanakodwera nazo zimene Dr Balogun anacita. Iwo anayamba ku mdzudzura kwambiri; Mwachisadzo, Molvi Ajmal Shahid, Mkulu wa Ahmadiyyah mu Nigeria amene anadabwa ifa ya mbale wace (ibid p.97) “Spiritual death” ndiponso Moulvi Naseem Saifi mkulu wa Ahmadiyyah ku mwera kwa Africa anasimikiza kuti Dr Balogun anasiya mpingo wa Ahmadiyyah natsata Chisilamu chi*****wa chimene iye anasiyira mphingo wa Ahmadiyyah.
Dr Balogun amene anaziwa Chisinsi cha Ahmadi ndi Usogoleri anayakha nati:
“Ndi kananena zonse mkulemba kwanga maka-maka (Usogoleri wa Palestini ahmadi) mkati-kati kopanda ku ulutsa, koma izi zikalembedwa mukangano pakati pa ife ndiponso akanachotsa mpingo. Mwa izi kulibe ena amene akanamva zimene ndinanena... Ene ndanena izi ndiganizo langa, Mulungu ndi kamboni wanga chi*****wa cha nchinto imene ndiri nawayo kwa abale anga mu Nigeria maka-maka asilamu ndiponso asilamu apadziko lapasi. Ganizo langa sikusutsa anthuwa a Ahmadiyya ai, ndakhala mphingo umeneu kwa dzaka zambiri, mukangano pa Islam ndi Ahmadiyyah, sinditaya nthawi kusankha Chisilamu” (Ibid p.17)
tikupempha kuti anthu Onse analowa mpingo wa Ahmadiyyah ayenera kuona chazoona maka-maka pa nkhani imene Dr Balogun alemba. Kodi iwo omwe agwilire ndi zionetsero za Quran, kaphuzisidwe ka Mtumiki Muhammad (SWA) ndiponso kuonetsa Chikondi ndi chikhupiriro mwa Mulungu.
Kwa okoda Mulungu obisara, (Amuna) m’njira ya mulungu, okoda mtumiki, pambuyo ya choonadi, sakutaya mulungu koma Mulungu aziwa zichitidwe zao kukhala zopanda phindu. (Quran, Muhammad 47:32)
Malemba Akuchokera mubuku: ‘Islam Versus Ahmadiyyah mu Nigeria,’ ofalitsa ndi Sh. Muhammad Ashraf, Kashmir Bazar Lahore Pakistani.
Idara Dawat-o-Irshad, USA, inc P.O. BOX 22885, Alexandrie VA 22304 http://www.irshad.org/idara/
Anti Ahmadiyya Movement in Islam Dr Syed Rashid Ali P.O. BOX 11560 Dibba Al-Fujairah United Arab Emirates http://alhafeez.org/rashid/ rasyed@emirates.net.ae